Jeremiah 5

Palibe Munthu Wolungama

1“Pitani uku ndi uku mʼmisewu ya Yerusalemu,
mudzionere nokha,
funafunani mʼmabwalo ake.
Ngati mungapeze munthu mmodzi
amene amachita zachilungamo ndi kufunafuna choonadi,
ndipo ndidzakhululukira mzinda uno.
2Ngakhale anthu akulumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’
komabe akungolumbira mwachinyengo.”

3Inu Yehova, kodi suja mumafuna anthu onena zoona?
Inu munawakantha anthuwo, koma sanamve kupweteka;
munawaphwanya anthuwo, koma sanatengepo phunziro.
Anawumitsa mitima yawo ngati mwala
ndipo anakaniratu kulapa.
4Ndiye ndinati, “Awa ndi amphawi chabe;
anthu ochita zopusa.
Sadziwa njira ya Yehova,
sazindikira zimene Mulungu wawo amafuna.
5Tsono ndidzapita kwa atsogoleri
ndi kukayankhula nawo;
ndithu iwo amadziwa njira ya Yehova,
amadziwa zomwe Mulungu wawo amafuna.”
Koma ayi, iwonso anathyola goli la Yehova
ndipo anadula msinga zawo.
6Choncho mkango wochokera ku nkhalango udzawapha,
mmbulu wochokera ku thengo udzawawononga,
kambuku adzawabisalira pafupi ndi mizinda yawo
kuti akhadzule aliyense amene adzayesera kutuluka mʼmizindamo
pakuti kuwukira kwawo ndi kwakukulu
ndipo abwerera mʼmbuyo kwambiri.

7Yehova akuti, “Kodi ndingakukhululukireni bwanji ndi zimene mwachita?
Ana anu andisiya Ine
ndipo amapembedza milungu imene si milungu konse.
Ine ndinawapatsa zonse zimene ankasowa,
komabe iwo anachita chigololo
namasonkhana ku nyumba za akazi achiwerewere.
8Monga amachitira akavalo onenepa akamamemesa,
aliyense wa iwo ankathamangira mkazi wa mnzake.
9Tsono ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi?”
akutero Yehova.
“Kodi nʼkuleka kuwulipsira
mtundu woterewu?

10“Pitani ku minda yake ya mipesa ndi kukayiwononga,
koma musakayiwononge kotheratu.
Sadzani nthambi zake
pakuti anthu amenewa si a Yehova.
11Nyumba ya Israeli ndi nyumba ya Yuda
onse akhala osakhulupirika kotheratu kwa Ine.”

12Iwowa ankanama ponena za Yehova kuti,
“Yehova sangachite zimenezi!
Choyipa sichidzatigwera;
sitidzaona nkhondo kapena njala.
13Mawu a aneneri azidzangopita ngati mphepo;
ndipo mwa iwo mulibe uthenga wa Yehova.
Choncho zimene amanena zidzawachitikira okha.”
14Chifukwa chake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse akuti,

“Popeza kuti anthu awa ayankhula mawu amenewa,
tsono mawu anga ndidzawasandutsa moto mʼkamwa mwako
ndipo anthu awa ndidzawasandutsa nkhuni zimene moto udzapserezeretu.
15Inu Aisraeli,” Yehova akuti,
“Ndikukubweretserani mtundu wa anthu ochokera kutali,
ndi mtundu umene sunagonjetsedwepo,
mtundu wakalekale umene chiyankhulo chawo inu simuchidziwa,
zimene akunena inu simungazimvetse.
16Zida zawo za nkhondo zapha anthu ambirimbiri;
onsewo ndi ankhondo amphamvu okhaokha.
17Adzakudyerani zokolola zanu ndi chakudya chanu,
adzapha ana anu aamuna ndi aakazi;
adzakupherani nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu,
adzawononga mpesa wanu ndi mikuyu yanu.
Ndi malupanga awo adzagwetsa
mizinda yanu yotetezedwa imene mumayidalira.
18“Komabe pa masiku amenewo sindidzakuwonongani kotheratu,” akutero Yehova. 19Ndipo pamene anthu adzafunsa Yehova kuti, “Chifukwa chiyani Yehova Mulungu wathu wachita zimenezi?” Iwe udzawawuze kuti, “Monga momwe mwasiyira Ine ndi kutumikira milungu yachilendo mʼdziko mwanu, momwemonso mudzatumikira anthu a mʼdzikonso lachilendo.”

20“Lengeza izi kwa ana a Yakobo
ndipo mulalikire kwa anthu a ku Yuda kuti,
21Imvani izi, inu anthu opusa ndi opanda nzeru,
inu amene maso muli nawo koma simupenya,
amene makutu muli nawo koma simumva.
22Kodi simuyenera kuchita nane mantha?”
Akutero Yehova.
“Kodi simuyenera kunjenjemera pamaso panga?
Ine ndinayika mchenga kuti ukhale malire a nyanja,
malire a muyaya amene nyanjayo singadutsepo.
Mafunde angawombe motani, koma sangathe kupitirira malirewo;
mafunde angakokome motani, koma sangadutse malirewo.
23Koma anthu awa ndi nkhutukumve ndiponso a mitima yowukira;
andifulatira ndipo andisiyiratu.
24Sananenepo mʼmitima mwawo kuti,
‘Tiyeni tizipembedza Yehova Mulungu wathu.
Kodi suja amatipatsa pa nthawi yake mvula yachizimalupsa ndi yamasika.
Iye salephera konse kutipatsa nyengo ya kholola.’
25Koma zolakwa zanu zalepheretsa zonsezi;
ndipo machimo anu akumanitsani zabwino.

26“Pakati pa anthu anga pali anthu ena oyipa
amene amabisalira anzawo monga amachitira mlenje mbalame
ndiponso ngati amene amatchera misampha kuti akole anthu anzawo.
27Nyumba zawo zadzaza ndi chuma chochipeza mwa chinyengo
ngati zikwere zodzaza ndi mbalame.
Nʼchifukwa chake asanduka otchuka ndi olemera.
28Ndipo ananenepa ndi kukhala ndi matupi osalala.
Ntchito zawo zoyipa nʼzopanda malire;
saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye kuti iyende bwino,
sateteza ufulu wa anthu osauka.
29Kodi Ine ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi?
Kodi ndisawulipsire
mtundu woterewu?
Akutero Yehova.

30“Chinthu chothetsa nzeru ndi choopsa kwambiri
chachitika mʼdzikomo:
31Aneneri akunenera zabodza,
ndipo ansembe akuvomerezana nawo,
ndipo anthu anga akukonda zimenezi.
Koma mudzatani potsiriza?
Copyright information for NyaCCL